Добавить новость
News in English
Новости сегодня

Новости от TheMoneytizer

Malawi ndi Zambia ikuthetsa miseche kudzera mwa DJ Kachamba ndi General Kanene

DJ Kachamba: mchitidwe wamiseche ukupangitsa kuti anthu ena adzikhala mopanda mtendere

Wabweranso DJ Kachamba, pano nde wabwera ndi General Kanene pomwe oyimba awiriwa anyamula mbendera ya Malawi ndi Zambia polimbana ndi mchitidwe wa mabodza mu nyimbo yatsopano Miseche.

Mu nyimboyi, awiriwa akuti mchitidwe wamiseche ndi umthira kuwiri ukupititsa pansi chitukuko cha maiko oyandikanawa.

Ngakhale izi zilo chomwechi, awiriwa akupempha mchitidwe oti anthu azimasukirana pakakhala kufunika kopereka chidzudzulo ‘osati kumwerana mowa kuti palalatidwe’.

Mwachitsanso DJ Kachamba wati mchitidwe wamiseche ukupangitsa kuti anthu ena adzikhala mopanda mtendere.

‘’Anthu ali pano, ndiovuta. Ndigule munda, ndzilima. Ati ndine okhwima. Ndigule galimoto nde mavuto onenedwa. Bola ndingolowera.’’ Ikutero nyimboyo.

General Kanene: anthu azimasukirana pakakhala kufunika kopereka chidzudzulo ‘osati kumwerana mowa kuti palalatidwe

Ndipo Kanene naye, wati ku Zambia anthu omwe sakondwera ena akamachita bwino aliko.

Komai ye wati, anthu omwe amanenedwa azilimbikirabe ndipo asafooke.

Nyimboyi yajambulidwa ku Favor Records ndi Elia Phiri.

Iye anati munyengo yonga iyiyi, anthu akuyenera kukhala ndi chidwi poti ena anangobadwa ndi mchitidwe obwezera anzawo mbuyo.

Pakadali pano, Kachamba wati apitiriza kutulutsa nyimbo zokamba mavuto omwe anthu amakumana nawo popereka njira zomwe angathanirane ndi mavutowa.

DJ Kachamba yemwe dzina lake ndi Simeone Masanjala, m’bale wa oyimba odziwika kuyambira kale Daniel Kachamba ndipo akukhala ku South Africa anatulutsa abamu ya nyimbo 11 yotchedwa Alipobe chaka chatha momwe munali nyimbo monga Chauta ndinso Maliro.

The post Malawi ndi Zambia ikuthetsa miseche kudzera mwa DJ Kachamba ndi General Kanene appeared first on Malawi Voice.

Читайте на сайте


Smi24.net — ежеминутные новости с ежедневным архивом. Только у нас — все главные новости дня без политической цензуры. Абсолютно все точки зрения, трезвая аналитика, цивилизованные споры и обсуждения без взаимных обвинений и оскорблений. Помните, что не у всех точка зрения совпадает с Вашей. Уважайте мнение других, даже если Вы отстаиваете свой взгляд и свою позицию. Мы не навязываем Вам своё видение, мы даём Вам срез событий дня без цензуры и без купюр. Новости, какие они есть —онлайн с поминутным архивом по всем городам и регионам России, Украины, Белоруссии и Абхазии. Smi24.net — живые новости в живом эфире! Быстрый поиск от Smi24.net — это не только возможность первым узнать, но и преимущество сообщить срочные новости мгновенно на любом языке мира и быть услышанным тут же. В любую минуту Вы можете добавить свою новость - здесь.




Новости от наших партнёров в Вашем городе

Ria.city
Музыкальные новости
Новости России
Экология в России и мире
Спорт в России и мире
Moscow.media






Топ новостей на этот час

Rss.plus





СМИ24.net — правдивые новости, непрерывно 24/7 на русском языке с ежеминутным обновлением *